Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 9:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo mwa nsoni zanu zochuluka simunawathe, kapena kuwataya; popeza Inu ndinu Mulungu wa chisomo ndi chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo mwa nsoni zanu zochuluka simunawatha, kapena kuwataya; popeza Inu ndinu Mulungu wa chisomo ndi chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Ngakhale zinali choncho, Inu simudaŵaononge kotheratu, kapena kuŵasiya, pakuti Inu ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Komabe mwachifundo chanu chachikulu simuwatheretu kapena kuwataya pakuti ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:31
15 Mawu Ofanana  

Koma Yehova analeza nao mtima, nawachitira chifundo, nawatembenukira; chifukwa cha chipangano chake ndi Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pake.


Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza chifundo pamaso pa iwo anawatenga ndende, nadzalowanso m'dziko muno; pakuti Yehova Mulungu wanu ngwa chisomo ndi chifundo; sadzakuyang'anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye.


nakana kumvera, osakumbukiranso zodabwitsa zanu munazichita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kunka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo; ndipo simunawasiye.


koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiye m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokere usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.


Chifukwa cha dzina langa ndidzachedwetsa mkwiyo wanga, ndi chifukwa cha kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakuchotse.


Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa.


Kwerani pa makoma ake nimupasule; koma musatsirize konse; chotsani nthambi zake pakuti sizili za Yehova.


Koma masiku onsewo, ati Yehova, sindidzatsirizitsa konse ndi iwe.


Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka,


Ambuye Mulungu wathu ndiye wachifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye;


popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wachifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala chipangano cha makolo anu chimene analumbirira iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa