Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 7:65 - Buku Lopatulika

65 Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka wauka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

65 Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka wauka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

65 Bwanamkubwa adaŵauza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya choperekedwa kwa Mulungu, mpaka wansembe wodziŵa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu atapezeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

65 Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 7:65
16 Mawu Ofanana  

Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka adzabuka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu.


Okhomera chizindikiro tsono ndiwo Nehemiya, Tirisata mwana wa Hakaliya, ndi Zedekiya,


Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawachotsa kuntchito ya nsembe.


Msonkhano wonse pamodzi ndiwo zikwi makumi anai ndi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi,


Ndipo ena a akulu a nyumba za makolo anapereka kuntchito. Kazembeyo anapereka kuchuma madariki agolide chikwi chimodzi, mbale zowazira makumi asanu, malaya a ansembe makumi atatu.


Ndipo Nehemiya, ndiye kazembe, ndi Ezara wansembe mlembiyo, ndi Alevi ophunzitsa anthu, ananena ndi anthu onse, Lero ndilo lopatulikira Yehova Mulungu wanu, musamachita maliro, musamalira misozi. Popeza anthu onse analira misozi pakumva mau a chilamulo.


Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa chapachifuwa cha chiweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula chiweruzo cha ana a Israele pamtima pake pamaso pa Yehova kosalekeza.


Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.


Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.


Asachiphike ndi chotupitsa. Ndachipereka chikhale gawo lao lochokera pa nsembe zanga zamoto; ndicho chopatulika kwambiri, monga nsembe yauchimo, ndi monga nsembe yopalamula.


Ndipo anamuika chapachifuwa; naika m'chapachifuwa Urimu ndi Tumimu.


Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa chiweruzo cha Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituluka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israele pamodzi naye, ndiwo khamu lonse.


Ndipo za Levi anati, Tumimu ndi Urimu wanu zikhala ndi wokondedwa wanu, amene mudamuyesa mu Masa, amene mudalimbana naye ku madzi a Meriba;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa