Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 7:64 - Buku Lopatulika

64 Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawachotsa kuntchito ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

64 Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawachotsa kuntchito ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

64 Iwoŵa adaafunafuna maina ao m'buku lolongosola kaundula wa mafuko ao, koma maina ao sadapezekemo. Choncho adaŵachotsa pa unsembe naŵaŵerenga kuti ngodetsedwa pa chipembedzo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

64 Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 7:64
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Aisraele onse anawerengedwa mwa chibadwidwe chao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israele; ndipo Yuda anatengedwa ndende kunka ku Babiloni chifukwa cha kulakwa kwao.


Muwakumbukire Mulungu wanga, popeza anadetsa unsembe, ndi pangano la unsembe, ndi la Alevi.


Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufulu, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa chibadwidwe chao. Ndipo ndinapeza buku la chibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo.


Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa ndi dzina lao.


Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka wauka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu.


akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa