Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 6:7 - Buku Lopatulika

7 Ndiponso waika aneneri akubukitsa za iwe ku Yerusalemu, ndi kuti, Ku Yuda kuli mfumu, ndipo zidzamveka kwa mfumu, kuti kuli zotere. Tiyeni tsono tipangane pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndiponso waika aneneri akubukitsa za iwe ku Yerusalemu, ndi kuti, Ku Yuda kuli mfumu, ndipo zidzamveka kwa mfumu, kuti kuli zotere. Tiyeni tsono tipangane pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Mwaikanso aneneri ku Yerusalemu oti azilengeza za inu kuti, ‘Ku Yuda kuli mfumu tsopano!’ Tsono zonsezi zimveka ndithu kwa mfumu ya ku Persiya. Choncho mubwere kuti tidzakambirane tonse pamodzi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mwayikanso kale aneneri amene adzalengeza za iwe mu Yerusalemu kuti ‘Mu Yuda muli mfumu!’ Tsono nkhani iyi imveka ndithu kwa mfumu. Choncho bwerani kuti tidzakambirane.”

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 6:7
10 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano taonani, Adoniya walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu simudziwa.


Popeza iye watsika lero, nakapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana aamuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abiyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pake, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya.


Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israele; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.


Ndipo anapangana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.


m'menemo mudalembedwa, Kwamveka mwa amitundu, ndi Gesemu achinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; chifukwa chake mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa.


Koma ndinamtumizira mau, akuti, Palibe zinthu zotere zonga unenazi, koma uzilingirira mumtima mwako.


Potero tsopano inu ndi bwalo la akulu a milandu muzindikiritse kapitao wamkulu kuti atsike naye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa