Nehemiya 6:6 - Buku Lopatulika6 m'menemo mudalembedwa, Kwamveka mwa amitundu, ndi Gesemu achinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; chifukwa chake mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 m'menemo mudalembedwa, Kwamveka mwa amitundu, ndi Gesemu achinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; chifukwa chake mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 M'kalatamo munali mau akuti, “Pakati pa mitundu ya anthu pano pamveka mphekesera, ndiponso Gesemu akunenanso momwemo, kuti inuyo, pamodzi ndi Ayuda, mukufuna kuukira boma. Nchifukwa chake mukumanganso khoma. Mukufuna kuti mukhale mfumu yao monga m'mene zikumvekeramu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Mu kalatamo munali mawu akuti, “Pali mphekesera pakati pa mitundu ya anthu, ndiponso Gesemu akunena zomwezo kuti inu ndi Ayuda onse mufuna kuwukira boma. Nʼchifukwa chake mukumanga khoma. Mphekeserazo zikutinso inu mukufuna kudzakhala mfumu yawo. Onani mutuwo |