Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 5:2 - Buku Lopatulika

2 Popeza panali ena akuti, Ife, ana athu aamuna ndi aakazi, ndife ambiri; talandira tirigu, kuti tidye tikhale ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Popeza panali ena akuti, Ife, ana athu aamuna ndi aakazi, ndife ambiri; talandira tirigu, kuti tidye tikhale ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Pakuti panali ena amene ankati, “Ife ndi ana athu tikuchuluka kwambiri, motero tikusoŵa tirigu wakudya, kuti tikhale ndi moyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ena ankanena kuti, “Ife ndi ana athu aamuna ndi aakazi, tilipo ochuluka kwambiri. Choncho tikufuna tirigu kuti tidye ndi kukhala ndi moyo.”

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 5:2
11 Mawu Ofanana  

Ndipo maiko onse anafika ku Ejipito kudzagula tirigu kwa Yosefe: chifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi.


Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti mu Ejipito muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe.


Ndipo Yuda anati kwa atate wake Israele, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.


tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? Mutigule ife ndi dziko lathu ndi chakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja.


Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake.


Panali enanso akuti, Tili kupereka chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa ndi nyumba zathu; kuti tilandire tirigu chifukwa cha njalayi.


Mwabzala zambiri, koma mututa pang'ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudziveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa ntchito yakulipidwa alandirira kulipirako m'thumba lobooka.


Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima.


Musamakongoletsa mbale wanu mopindulitsa; phindu la ndalama, phindu la chakudya, phindu la kanthu kalikonse kokongoletsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa