Nehemiya 5:18 - Buku Lopatulika18 Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng'ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundumitundu; chinkana chonsechi sindinafunsire chakudya cha kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng'ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundumitundu; chinkana chonsechi sindinafunsira chakudya cha kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Tsono chakudya cha pa tsiku limodzi chinali ichi: ng'ombe imodzi, nkhosa zisanu ndi imodzi zonenepa, ndiponso nkhuku zochuluka. Pa masiku khumi aliwonse panalinso matumba achikopa ochuluka a vinyo. Komabe ngakhale choncho, ine sindidafune kulandira chakudya chimene abwanamkubwa ankalandira, chifukwa chakuti anthu anga anali othinidwa kwambiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Tsiku lililonse pamaphikidwa ngʼombe imodzi, nkhosa zabwino zisanu ndi imodzi pamodzi ndi nkhuku. Ndipo pakutha pa masiku khumi aliwonse pankakhala matumba achikopa ochuluka a vinyo wa mitundu yonse. Ngakhale zinali choncho, Ine sindinatenge chakudya choperekedwa kwa bwanamkubwa, chifukwa izi zinali zosautsa anthu. Onani mutuwo |