Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 5:17 - Buku Lopatulika

17 Panalinso podyera ine Ayuda ndi olamulira amuna zana limodzi mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kuchokera kwa amitundu otizinga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Panalinso podyera ine Ayuda ndi olamulira amuna zana limodzi mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kuchokera kwa amitundu otizinga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Komanso masiku onse ndinkadyetsa anthu 150, Ayuda ndi akulu olamula, kuphatikizapo anthu amene adaabwera kwa ife kuchokera kwa mitundu ina yotizungulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Kuwonjezera apa, ndinkadyetsa Ayuda, akuluakulu kuphatikizanso anthu amene ankabwera kwa ife kuchokera kwa mitundu ya anthu otizungulira okwanira 150.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 5:17
8 Mawu Ofanana  

Chomwecho Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ake onse awiri.


Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.


Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisraele onse kuphiri la Karimele, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a chifanizocho mazana anai, akudya pa gome la Yezebele.


Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wake nyumba, chifukwa cha nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ake.


Ndiponso ndinalimbikira ntchito ya linga ili, ngakhale dziko sitinaligule, ndi anyamata anga onse anasonkhanira ntchito komweko.


Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe.


Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa