Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 4:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira ntchito, ndi gawo lina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi malaya achitsulo; ndi akulu anali m'mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira ntchito, ndi gawo lina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi malaya achitsulo; ndi akulu anali m'mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake, theka lina la antchito anga linkagwira ntchitoyo, ndipo theka lina linkagwira mikondo, zishango, mauta ndiponso linkavala malaya achitsulo. Tsono akulu a Ayuda ankalimbitsa anthu ao amene ankamanga khoma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo mwake, theka la antchito anga linkagwira ntchito, pamene theka linalo limatenga mikondo, zishango, mauta ndi kuvala malaya azitsulo. Akuluakulu ankalimbikitsa Ayuda onse

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 4:16
8 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pakumva adani athu kuti chinadziwika nafe, ndi kuti Mulungu adapititsa pachabe uphungu wao, tinabwera tonse kunka kulinga, yense kuntchito yake.


Iwo omanga linga, ndi iwo osenza katundu, posenza, anachita aliyense ndi dzanja lake lina logwira ntchito, ndi lina logwira chida;


Ndipo ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, angakhale amuna olindirira onditsata ine, nnena mmodzi yense wa ife anavula zovala zake, yense anapita ndi chida chake kumadzi.


Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine; iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.


Ndipo polowa mutu pakhale pakati pake; pakhale mkawo pozungulira polowa pake, wa ntchito yoomba, ngati polowa pa malaya otchinjiriza, pangang'ambike.


Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo: Yense ali ndi lupanga lake pantchafu pake, chifukwa cha upandu wa usiku.


Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zazitsulo; tuulani nthungo zanu, valani malaya achitsulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa