Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 4:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo kunali, pakumva adani athu kuti chinadziwika nafe, ndi kuti Mulungu adapititsa pachabe uphungu wao, tinabwera tonse kunka kulinga, yense kuntchito yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo kunali, pakumva adani athu kuti chinadziwika nafe, ndi kuti Mulungu adapititsa pachabe uphungu wao, tinabwera tonse kunka kulinga, yense kuntchito yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Pamene adani athu adamva kuti ife tikudziŵa cholinga chao, adazindikira kuti Mulungu walepheretsa zimene iwowo adaapangana kuti atichite. Tsono tonse tidapitanso ku ntchito yomanga khoma, aliyense ku ntchito yake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Adani athu atamva kuti ife tadziwa za chiwembu chawo, anadziwanso kuti Yehova walepheretsa zimene ankafuna kutichita. Choncho tinabwerera aliyense ku ntchito yake yomanga khoma.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 4:15
13 Mawu Ofanana  

Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.


Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.


Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira ntchito, ndi gawo lina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi malaya achitsulo; ndi akulu anali m'mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Ndine amene nditsutsa zizindikiro za matukutuku, ndi kuchititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m'mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao:


Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mau, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.


Monga ngati munthu wa paulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamula wapakhomo adikire.


musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye;


ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa