Nehemiya 4:14 - Buku Lopatulika14 Ndipo ndinapenya, ndinanyamuka, ndinanena kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Musamawaopa iwo; kumbukirani Ambuye wamkulu ndi woopsa, ndi kuponyera nkhondo abale anu, ana anu aamuna ndi aakazi, akazi anu, ndi nyumba zanu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Ndipo ndinapenya, ndinanyamuka, ndinanena kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Musamawaopa iwo; kumbukirani Yehova wamkulu ndi woopsa, ndi kuponyera nkhondo abale anu, ana anu aamuna ndi aakazi, akazi anu, ndi nyumba zanu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Koma nditazindikira mantha ao, ndidachitapo kanthu. Mwakuti ndidauza atsogoleri ndi akulu olamula, ndiponso anthu ena onse kuti, “Musaŵaope ameneŵa. Kumbukirani kuti Chauta ndi wamkulu ndiponso ndi woopsa, tsono mumenyere nkhondo abale anu, ana anu, akazi anu, ndi nyumba zanu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Popeza anthu ankachita mantha, tsono ndinawawuza anthu olemekezeka, akuluakulu ndiponso anthu onse kuti, “Musawaope. Kumbukirani kuti Ambuye ndi wamkulu ndipo ndi woopsa. Choncho menyerani nkhondo abale anu, ana aamuna ndi aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.” Onani mutuwo |