Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 3:26 - Buku Lopatulika

26 Koma antchito a m'kachisi okhala mu Ofele anakonza kufikira kumalo a pandunji pa Chipata cha Madzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Koma Anetini okhala m'Ofele anakonza kufikira kumalo a pandunji pa Chipata cha Madzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 ndi atumiki a ku Nyumba ya Mulungu, amene ankakhala pa khoma la Ofele, adakonza chigawo china mpaka ku malo oyang'anana ndi Chipata cha Madzi kuvuma, ndiponso nsanja yaitali ija.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 ndi otumikira mʼNyumba ya Mulungu amene amakhala pa khoma la Ofeli anakonza chigawo china mpaka pa malo oyangʼanana ndi Chipata cha Madzi kuloza kummawa ndiponso nsanja yayitali ija.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 3:26
13 Mawu Ofanana  

Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwaomwao m'mizinda mwao, ndiwo Israele, ansembe, Alevi, ndi Antchito a m'kachisi.


Anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova, ndi pa linga la Ofele anamanga kwakukulu.


Chitatha ichi tsono iye anaumangira mzinda wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'chigwa, mpaka polowera pa Chipata cha Nsomba; nazinga Ofele, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'mizinda yonse yamalinga ya mu Yuda.


Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oimbira, antchito a m'kachisi, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata chilamulo cha Mulungu, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, yense wodziwa ndi wozindikira,


Koma antchito a m'kachisi anakhala mu Ofele, ndi Ziha, ndi Gisipa anali oyang'anira antchito a m'kachisi.


ndi ku Chipata cha ku Chitsime, ndi kundunji kwao, anakwerera pa makwerero a mzinda wa Davide, potundumuka linga, popitirira pa nyumba ya Davide, mpaka ku Chipata cha Madzi kum'mawa.


Potsatizana nao Atekowa anakonza gawo lina, pandunji pa nsanja yaikulu yosomphoka ndi kulinga la Ofele.


Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi kukhwalala lili ku Chipata cha Madzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la chilamulo cha Mose, chimene Yehova adalamulira Israele.


Natuluka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yake, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la Chipata cha Madzi, ndi pa khwalala la Chipata cha Efuremu.


Nawerenga m'menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo.


pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mzinda wa anthu ambiri udzakhala bwinja; chitunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba kunthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa