Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 3:25 - Buku Lopatulika

25 Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene ili kubwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene ili kubwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 ndiponso mpaka ku ngodya. Palala, mwana wa Uzai, adakonza chigawo china choyang'anana ndi Ndonyo ndiponso ndi nsanja yotuluka pa nyumba yapamwamba ya mfumu ku bwalo la alonda. Pambali pa iyeyo Pedaya, mwana wa Parosi,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Palali mwana Uzai anakonza chigawo china choyangʼanana ndi ngodya ndi nsanja yotuluka pa nyumba yapamwamba ya mfumu ku bwalo la alonda. Motsatana naye, Pedaya mwana wa Parosi,

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 3:25
12 Mawu Ofanana  

ana a Parosi, zikwi ziwiri ndi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.


ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata cha Nsomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka ku Chipata cha Nkhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.


ana a Parosi zikwi ziwiri mphambu zana limodzi kudza makumi asanu ndi awiri.


Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo; ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.


amene ati, Ndidzadzimangira ndekha nyumba yotakata ndi zipinda zapamwamba zazikulu, nadziboolera mazenera; navundikira tsindwi lam'kati ndi mikungudza, naipaka ndi utoto wofiira.


Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babiloni inamangira Yerusalemu misasa; ndipo Yeremiya mneneri anatsekeredwa m'bwalo la kaidi, linali kunyumba ya mfumu ya Yuda.


Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya nthawi yachiwiri, pamene iye anali chitsekedwere m'bwalo la kaidi, kuti,


Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m'bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma kumseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m'mzinda. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi.


Ndipo anamkweza Yeremiya ndi zingwe, namtulutsa m'dzenjemo; ndipo Yeremiya anakhalabe m'bwalo la kaidi.


Ndipo Ababiloni anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.


Ndipo iwe, nsanja ya nkhosa, chitunda cha mwana wamkazi wa Ziyoni, udzafikira iwe, inde udzafika ulamuliro wakale, ufumu wa mwana wamkazi wa Yerusalemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa