Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 2:6 - Buku Lopatulika

6 Ninena nane mfumu, ilikukhala pansi pamodzi ndi mkazi wake wamkulu, Ulendo wako ngwa nthawi yanji, udzabweranso liti? Ndipo kudakonda mfumu kunditumiza nditaitchula nthawi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ninena nane mfumu, ilikukhala pansi pamodzi ndi mkazi wake wamkulu, Ulendo wako ngwa nthawi yanji, udzabweranso liti? Ndipo kudakonda mfumu kunditumiza nditaitchula nthawi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Apo mfumu, mkazi wake ali pambali pake, idandifunsa kuti, “Kodi kumeneko ukakhalako nthaŵi yaitali bwanji, ndipo udzabwerako liti?” Ndidaiwuza nthaŵi yake, ndipo idandilola kuti ndipite.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Tsono mfumu, mfumukazi itakhala pambali pake, anandifunsa kuti, “Kodi kumeneko ukakhalako masiku angati ndipo udzabwera liti?” Ndinayiwuza mfumu nthawi yake ndipo inandilola kuti ndipite.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 2:6
9 Mawu Ofanana  

Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.


Koma pochitika ichi chonse sindinkakhale ku Yerusalemu; pakuti chaka cha makumi atatu ndi chachiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu ya Babiloni ndinafika kwa mfumu, ndipo atapita masiku ena ndinapempha mfumu indilole;


Ndipo mfumu inati kwa ine, Ufunanji iwe? Pamenepo ndinapemphera Mulungu wa Kumwamba.


Ndipo ndinati kwa mfumu, Chikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda kumzinda wa manda a makolo anga, kuti ndiumange.


Ndipo chiyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m'dziko la Yuda; kuyambira chaka cha makumi awiri kufikira chaka cha makumi atatu mphambu ziwiri cha Arita-kisereksesi mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadye chakudya cha kazembe.


Ndipo iwo amene adzakhala a iwe adzamanga malo akale abwinja; udzautsa maziko a mibadwo yambiri; udzatchedwa Wokonza pogumuka, Wakubwezera njira zakukhalamo.


Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso mizinda yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri.


Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.


Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa