Nehemiya 2:5 - Buku Lopatulika5 Ndipo ndinati kwa mfumu, Chikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda kumzinda wa manda a makolo anga, kuti ndiumange. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo ndinati kwa mfumu, Chikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda kumudzi wa manda a makolo anga, kuti ndiumange. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Ndipo ndidaiwuza mfumuyo kuti, “Ngati chingakukondweretseni amfumu, ndipo ngati mungandikomere mtima mtumiki wanune, munditume ku Yuda, kumzinda kumene kuli manda a makolo anga, kuti ndikaumangenso mzindawo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Ndipo ndinayankha kuti, “Ngati amfumu chingakukondweretseni, ngati mungakomere mtima mtumiki wanune, mundilole kuti ndipite ku Yuda, ku mzinda kumene kuli manda a makolo anga kuti ndikawumangenso.” Onani mutuwo |