Nehemiya 13:5 - Buku Lopatulika5 namkonzera chipinda chachikulu, kumene adasungira kale zopereka za ufa, lubani, ndi zipangizo, ndi limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamulidwira Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 namkonzera chipinda chachikulu, kumene adasungira kale zopereka za ufa, lubani, ndi zipangizo, ndi limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamulidwira Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 adakonzera Tobiyayo chipinda chachikulu m'mene kale ankasungiramo zopereka zaufa, lubani, ziŵiya, mphatso zoyenerera ansembe, ndiponso zopereka za chachikhumi cha chakudya, vinyo ndi mafuta, zimene adaalamula kuti azipatse Alevi, anthu oimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, potsata malamulo a Mose. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Choncho anamupatsa chipinda chachikulu chimene kale ankasungamo zopereka zakudya, lubani, ziwiya, zopereka za chakhumi za tirigu, vinyo ndi mafuta zoyenera kuperekedwa kwa Alevi, oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, komanso mphatso zoyenera kupereka kwa ansembe. Onani mutuwo |
ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uliwonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, kuzipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzilimodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife.