Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 13:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo kunali, atamva chilamulocho, anasiyanitsa pa Israele anthu osokonezeka onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo kunali, atamva chilamulocho, anasiyanitsa pa Israele anthu osokonezeka onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono pamene anthuwo adamva lamulolo, adachotsa anthu onse achilendo pakati pa gulu lao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Anthu atamva lamuloli, anachotsa pakati pawo onse amene anali achilendo.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 13:3
12 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake tsono, wululani kwa Yehova Mulungu wa makolo anu, nimuchite chomkondweretsa; mudzilekanitse ndi mitundu ya anthu a m'dzikomo, ndi kwa akazi achilendo.


Pakuti anadzitengera okha ndi ana aamuna ao ana aakazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.


Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oimbira, antchito a m'kachisi, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata chilamulo cha Mulungu, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, yense wodziwa ndi wozindikira,


Nadzipatula a mbumba ya Israele kwa alendo onse, naimirira, nawulula zochimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.


Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.


Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu.


Ndipo anthu ambiri osokonezeka anakwera nao; ndi nkhosa ndi ng'ombe, zoweta zambirimbiri.


Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.


Ndipo anthu osokonezeka ali pakati pao anagwidwa nacho chilakolako; ndi ana a Israele omwe analiranso, nati, Adzatipatsa nyama ndani?


chifukwa kuti pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.


Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa