Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 13:2 - Buku Lopatulika

2 popeza sanawachingamire ana a Israele ndi chakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 popeza sanawachingamire ana a Israele ndi chakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Paja ameneŵa sadapite kukakomana ndi ana a Aisraele, kuti akaŵapatse buledi ndi madzi. M'malo mwake adalemba Balamu kuti aŵatemberere. Komabe Mulungu wathu matembererowo adaŵasandutsa madalitso.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Paja iwowa sanawachingamire Aisraeli kukawapatsa chakudya ndi madzi. Mʼmalo mwake analemba ganyu Baalamu kuti adzawatemberere. Komabe Mulungu wathu anasandutsa tembererolo kukhala mdalitso.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 13:2
12 Mawu Ofanana  

Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu; pakuuka iwowa adzachita manyazi, koma mtumiki wanu adzakondwera.


Anthu anga, kumbukiranitu chofunsira Balaki mfumu ya Mowabu, ndi chomuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.


Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ukani, Balaki, imvani; ndimvereni, mwana wa Zipori.


Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.


Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;


popeza sanakumane nanu ndi mkate ndi madzi m'njira muja munatuluka mu Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni.


Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.


posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa