Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 12:47 - Buku Lopatulika

47 Ndi Aisraele onse m'masiku a Zerubabele, ndi m'masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

47 Ndi Aisraele onse m'masiku a Zerubabele, ndi m'masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

47 Pa nthaŵi ya Zerubabele ndi Nehemiya, anthu a m'dziko lonse la Israele ankapereka tsiku ndi tsiku mphatso zofunika kwa anthu oimba nyimbo ndiponso kwa alonda a ku Nyumba ya Mulungu. Ankaikanso padera chigawo cha Alevi, ndipo Aleviwo nawonso ankaika padera chigawo cha ansembe, adzukulu a Aroni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

47 Choncho mu nthawi ya Zerubabeli ndi Nehemiya, Aisraeli onse anakapereka mphatso tsiku ndi tsiku kwa anthu oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu. Ankayikanso padera chigawo cha zopereka cha Alevi. Nawonso Alevi ankayika padera chigawo cha zopereka cha ansembe, zidzukulu za Aaroni.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 12:47
14 Mawu Ofanana  

Ndi kunena za chakudya chake, panali chakudya chosalekeza chopatsidwa kwa iye ndi mfumu, tsiku lililonse gawo lake, masiku onse a moyo wake.


Nadza iwo, naitana mlonda wa mzinda, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi abulu omanga, ndi mahema ali chimangire.


ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israele ndiko:


Pakuti mfumu inalamulira za iwowa, naikira oimbira chowathandiza, yense chake pa tsiku lake.


Ndipo ansembe ndi Alevi amene anakwera ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa, ndi awa: Seraya, Yeremiya, Ezara,


Ndi m'masiku a Yoyakimu ansembe aakulu a nyumba za makolo ndiwo: wa Seraya, Meraya; wa Yeremiya, Hananiya;


Awa anakhala m'masiku a Yoyakimu mwana wa Yesuwa, mwana wa Yozadaki, ndi m'masiku a Nehemiya kazembe, ndi a Ezara wansembe mlembiyo.


Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m'zonse zabwino.


Chakudya chao chizifanana, osawerengapo zolowa zake zogulitsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa