Nehemiya 12:44 - Buku Lopatulika44 Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za chuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzilimodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi chilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi akuimirirako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201444 Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za chuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzilimodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi chilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi akuimirirako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa44 Tsiku limenelo padasankhidwa anthu oyang'anira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, ndi zopereka zachikhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka potsata Malamulo a Mose, kuti azipereka kwa ansembe ndi Alevi, kuchokera ku minda ya midzi yonse. Pakuti Ayuda ankakondwera nawo ansembe ndi Alevi otumikirawo, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero44 Tsiku limenelo panasankhidwa anthu oyangʼanira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, zopereka za chakhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka kuchokera ku minda ya midzi yonse kuti azipereke kwa ansembe ndi Alevi malingana ndi malamulo. Izi zinali chomwechi chifukwa Ayuda ankakondwera ndi utumiki wa ansembe ndi Alevi. Onani mutuwo |