Nehemiya 12:43 - Buku Lopatulika43 Ndipo anaphera nsembe zambiri tsiku lija, nasekerera; pakuti Mulungu anawakondweretsa ndi chimwemwe chachikulu; ndi akazi omwe ndi ana anakondwera; ndi chikondwerero cha Yerusalemu chinamveka kutali. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201443 Ndipo anaphera nsembe zambiri tsiku lija, nasekerera; pakuti Mulungu anawakondweretsa ndi chimwemwe chachikulu; ndi akazi omwe ndi ana anakondwera; ndi chikondwerero cha Yerusalemu chinamveka kutali. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa43 Pa tsiku limenelo anthu adapereka nsembe zochuluka, ndipo adakondwa kwakukulu, popeza kuti Mulungu ndiye adaŵakondwetsa. Akazi nawonso, pamodzi ndi ana, adakondwa, ndipo kukondwa kwa anthu a ku Yerusalemu kudamveka patali. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero43 Pa tsiku limenelo anthu anapereka nsembe zambiri ndipo anakondwera chifukwa Mulungu anawapatsa chimwemwe chachikulu. Nawonso akazi ndi ana anakondwera ndipo kukondwa kwa anthu a mu mzinda wa Yerusalemu kunamveka kutali. Onani mutuwo |
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.