Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 11:30 - Buku Lopatulika

30 Zanowa, Adulamu ndi midzi yao, Lakisi ndi minda yake, Azeka ndi midzi yake. Ndipo anamanga misasa kuyambira ku Beereseba mpaka chigwa cha Hinomu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Zanowa, Adulamu ndi midzi yao, Lakisi ndi minda yake, Azeka ndi milaga yake. Ndipo anamanga misasa kuyambira ku Beereseba mpaka chigwa cha Hinomu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Zanowa, Adulamu ndi midzi yake. Ankakhalanso ku Lakisi ndi ku minda yake, ku Azeka ndi midzi yake. Motero ankakhala m'midzi yonse kuyambira ku Beereseba mpaka ku chigwa cha Hinomu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Zanowa, Adulamu ndi midzi yake, ku Lakisi ndi minda yake, ku Beeriseba mpaka ku chigwa cha Hinomu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 11:30
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.


ana a Ismaele ndi awa: maina ao m'midzi yao, m'misasa yao ndi awa: akalonga khumi ndi awiri m'mitundu yao.


Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'chigwa cha ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.


ndi mu Enirimoni, ndi mu Zora, ndi mu Yaramuti,


Ana a Benjamini omwe, kuyambira ku Geba pa Mikimasi, ndi Aya, ndi pa Betele ndi midzi yake,


Chipata cha ku Chigwa anachikonza Hanuni; ndi okhala mu Zanowa anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso mikono chikwi chimodzi cha lingalo mpaka ku Chipata cha Kudzala.


Ndipo kazembeyo anabwerera, napeza mfumu ya Asiriya ilikuponyana nkhondo ndi Libina; pakuti anamva kuti inachoka ku Lakisi.


nutulukire kuchigwa cha mwana wake wa Hinomu, chimene chili pa khomo la Chipata cha Mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe;


chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova kuti pamalo pano sipadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wake wa Hinomu, koma Chigwa Chophera anthu.


Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m'chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene sindinawauze, chimene sichinalowe m'mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.


Ndidzakutengeranso wokhala mu Maresa iwe, iye amene adzakulandira ukhale cholowa chake; ulemerero wa Israele udzafikira ku Adulamu.


Chifukwa chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anatuma kwa Hohamu, mfumu ya Hebroni, ndi kwa Piramu mfumu ya Yaramuti, ndi kwa Yafiya mfumu ya Lakisi, ndi kwa Debiri mfumu ya Egiloni, ndi kuti,


mfumu ya ku Libina, imodzi; mfumu ya ku Adulamu, imodzi;


Lakisi ndi Bozikati ndi Egiloni;


nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto.


natsikira malire kunka polekezera phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha mwana wa Hinomu, ndicho cha m'chigwa cha Refaimu kumpoto; natsikira ku chigwa cha Hinomu, ku mbali ya Ayebusi kumwera, natsikira ku Enirogele;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa