Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 11:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo akulu a anthu anakhala mu Yerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale mu Yerusalemu, mzinda wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m'mizinda ina.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo akulu a anthu anakhala m'Yerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale m'Yerusalemu, mudzi wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m'midzi ina.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Nthaŵi imeneyo atsogoleri a mabanja a Aisraele ankakhala ku Yerusalemu. Tsono anthu ena onse adachita maele kuti apeze munthu mmodzi pa anthu khumi aliwonse oti azikhala ku Yerusalemu, mzinda wopatulikawo, ndipo anthu asanu ndi anai otsala azikhalabe m'midzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Nthawi imeneyo atsogoleri a anthu ankakhala ku Yerusalemu. Tsono anthu ena onse anachita maere kuti apeze munthu mmodzi pa anthu khumi aliwonse kuti azikhala ku Yerusalemu, mzinda wopatulika. Anthu asanu ndi anayi otsalawo ankakhala mʼmidzi yawo.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 11:1
21 Mawu Ofanana  

Ndipo anachita maere, ang'ono ndi akulu, monga mwa nyumba za makolo ao, kuchitira zipata zonse.


Awa ndi akulu a nyumba za makolo mwa mibadwo yao, ndiwo akulu anakhala mu Yerusalemu awa.


Ndipo Aisraele onse anawerengedwa mwa chibadwidwe chao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israele; ndipo Yuda anatengedwa ndende kunka ku Babiloni chifukwa cha kulakwa kwao.


Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwaomwao m'mizinda mwao, ndiwo Israele, ansembe, Alevi, ndi Antchito a m'kachisi.


Ndipo mu Yerusalemu munakhala a ana a Yuda, ndi a ana a Benjamini, ndi a ana a Efuremu ndi Manase:


Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a chopereka cha nkhuni, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika chaka ndi chaka, kuzisonkha paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'chilamulo;


Alevi onse m'mzinda wopatulikawo ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu kudza anai.


Ndinanenanso kwa anthu nthawi yomweyi, Aliyense agone mu Yerusalemu pamodzi ndi mnyamata wake, kuti atilindirire usiku, ndi kugwira ntchito usana.


Pakuti pamenepo anaika mipando ya chiweruzo, mipando ya nyumba ya Davide.


Mupempherere mtendere wa Yerusalemu; akukonda inu adzaona phindu.


Maere aponyedwa pamfunga; koma ndiye Yehova alongosola zonse.


Pakuti adziyesa okha a mzinda wopatulika, ndi kudzikhazikitsa iwo okha pa Mulungu wa Israele; dzina lake ndi Yehova wa makamu.


Galamuka! Galamuka! Tavala mphamvu zako, Ziyoni; tavala zovala zako zokongola, Yerusalemu, mzinda wopatulika; pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso kwa iwe wosadulidwa ndi wodetsedwa.


ndipo anatuluka m'manda mwao pambuyo pa kuuka kwake, nalowa m'mzinda woyera, naonekera kwa anthu ambiri.


Pamenepo mdierekezi anamuka naye kumzinda woyera; namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisi,


Ndipo anapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikira mitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri mmodziyo amene munamsankha,


Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiasi; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.


Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israele dziko, monga mwa magawo ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa