Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 10:39 - Buku Lopatulika

39 Pakuti ana a Israele ndi ana a Levi, azibwera nayo nsembe yokweza yatirigu, ndi yavinyo ndi yamafuta, kuzipinda kuli zipangizo za malo opatulika, ndi ansembe akutumikira, ndi odikira, ndi oimbira; kuti tisasiye nyumba ya Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Pakuti ana a Israele ndi ana a Levi, azibwera nayo nsembe yokweza yatirigu, ndi yavinyo ndi yamafuta, kuzipinda kuli zipangizo za malo opatulika, ndi ansembe akutumikira, ndi odikira, ndi oimbira; kuti tisasiye nyumba ya Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Aisraele ndiponso a m'banja la Levi adzapereka tirigu, vinyo ndi mafuta kuzipinda kosungira ziŵiya za m'malo opatulika, ndiponso kokhala ansembe amene akutumikira, pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, ndi anthu oimba nyimbo. Ndithu ife tidzasamala Nyumba ya Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Choncho Israeli, kuphatikiza zidzukulu za Alevi, azipititsa zopereka za tirigu, vinyo ndi mafuta ku zipinda zosungiramo katundu wopatulika, komanso kokhala ansembe amene akutumikira pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu ndi anthu oyimba nyimbo. “Kwambiri ife sitidzaleka kusamala Nyumba ya Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 10:39
12 Mawu Ofanana  

Nadza iwo, naitana mlonda wa mzinda, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi abulu omanga, ndi mahema ali chimangire.


Pamenepo Hezekiya anawauza akonze zipinda m'nyumba ya Yehova; nazikonza.


Ndipo anabwera nazo nsembe zokweza, ndi amodzi a magawo khumi, ndi zinthu zopatulika, mokhulupirika; ndi mkulu woyang'anira izi ndiye Konaniya Mlevi, ndi Simei mng'ono wake ndiye wotsatana naye.


Ndi Aisraele onse m'masiku a Zerubabele, ndi m'masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni.


Chifukwa cha nyumba ya Yehova Mulungu wathu ndidzakufunira zokoma.


Unenenso ndi Alevi, nuti nao, Pamene mulandira kwa ana a Israele, limodzi la magawo khumi limene ndakupatsani likhale cholowa chanu chochokera kwao, muziperekako nsembe yokweza ya Yehova, limodzi la magawo khumi la limodzi la magawo khumi.


Chifukwa chake unene nao, Pamene mukwezako zokometsetsa zake, zidzayesedwanso kwa Alevi ngati zipatso za padwale, ndi zipatso za mopondera mphesa.


Simungathe kudya m'mudzi mwanu limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, kapena la vinyo wanu, kapena la mafuta anu, kapena oyamba kubadwa a ng'ombe zanu kapena la nkhosa ndi mbuzi zanu, kapena zowinda zanu zilizonse muzilonjeza kapena nsembe zanu zaufulu, kapena nsembe yokweza ya m'dzanja lanu;


osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa