Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 10:38 - Buku Lopatulika

38 Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzilimodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzilimodzi la magawo khumi kunyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, kunyumba ya chuma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzilimodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzilimodzi la magawo khumi kunyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, kunyumba ya chuma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Wansembe, mdzukulu wa Aroni, adzakhale pamodzi ndi Alevi, pamene Aleviwo akulandira zigawo zachikhumizo. Ndipo Alevi adzabwera ndi zigawozo ku Nyumba ya Mulungu wathu, ku zipinda zosungiramo katundu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Wansembe, mdzukulu wa Aaroni azikhala pamodzi ndi Alevi pamene akulandira chakhumi. Ndipo Alevi azibwera ndi chakhumicho ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda zosungiramo chuma.”

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 10:38
11 Mawu Ofanana  

pakuti odikira anai aakulu, ndiwo Alevi, anali mu udindo wao, nayang'anira zipinda ndi mosungiramo chuma m'nyumba ya Mulungu.


ndi chopereka cha nkhuni pa nthawi zoikika, ndi wa zipatso zoyamba. Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.


Limodzi mwa magawo khumi la zonse m'dziko, la mbeu zake za dziko, la zipatso za mtengo, ndilo la Yehova; likhale lopatulikira Yehova.


kudzali, pakudya inu mkate wa m'dzikolo, muzikwezera Yehova nsembe yokweza.


Muzipatsa Yehova nsembe yokweza yoitenga ku mtanda wanu woyamba, mwa mibadwo yanu.


Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse mu Israele, likhale cholowa chao, mphotho ya pa ntchito yao alikuichita, ntchito ya chihema chokomanako.


Popeza ndapatsa Alevi limodzi la magawo khumi, la ana a Israele, limene apereka nsembe yokweza kwa Yehova, likhale cholowa chao; chifukwa chake ndanena nao, Asadzakhale nacho cholowa mwa ana a Israele.


Muzipereka ndithu limodzi la magawo khumi la zipatso zonse za mbeu zanu, zofuma kumunda, chaka ndi chaka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa