Nehemiya 10:34 - Buku Lopatulika34 Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a chopereka cha nkhuni, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika chaka ndi chaka, kuzisonkha paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'chilamulo; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201434 Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a chopereka cha nkhuni, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika chaka ndi chaka, kuzisonkha pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'chilamulo; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa34 Ife ansembe, Alevi ndi anthu wamba tidzachita maele, kuti tisankhe mabanja amene adzapereke nkhuni ndi kubwera nazo ku Nyumba ya Mulungu wathu, pa nthaŵi zake zoikidwa, chaka ndi chaka, kuti azipserezera nsembe za pa guwa la Chauta, Mulungu wathu, monga mudalembedwera m'Malamulo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero34 “Ife ansembe, Alevi ndi anthu onse, tachita maere kuti tidziwe pamene banja lathu lililonse lidzabweretsa ku nyumba ya Mulungu wathu pa nthawi yoyikika ya chaka zopereka za nkhuni zoyaka pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo.” Onani mutuwo |