33 kulipereka mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israele zoipa, ndi ntchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.
33 kulipereka mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israele zoipa, ndi ntchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.
33 Tiziperekanso ndalama zolipirira buledi woperekedwa, chopereka cha chakudya ndiponso nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku, zopereka za pa masabata, za pokhala mwezi, za pa masiku achikondwerero osankhidwa, zoperekera zinthu zopatulika ndiponso nsembe zopepesera machimo a Aisraele, kudzanso zoperekera china chilichonse chofunika pa ntchito ya ku Nyumba ya Mulungu.
33 Ndalamayi izithandiza kulipirira buledi wa pa tebulo, chopereka cha chakudya cha nthawi zonse, zopereka zopsereza za nthawi zonse, zopereka za pa tsiku la Sabata, za pachikondwerero cha Mwezi Watsopano, za pa masiku a chikondwerero osankhika, zopereka za zinthu zopatulika, zopereka za nsembe yopepesera machimo a Aisraeli ndi ntchito ina iliyonse ya ku Nyumba ya Mulungu.
Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele.
Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.