Mlaliki 9:2 - Buku Lopatulika2 Zonse zigwera onse chimodzimodzi; kanthu kamodzi kangogwera wolungama ndi woipa; ngakhale wabwino ndi woyera ndi wodetsedwa; ngakhale wopereka nsembe ndi wosapereka konse; wabwino alingana ndi wochimwa; wolumbira ndi woopa lumbira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Zonse zigwera onse chimodzimodzi; kanthu kamodzi kangogwera wolungama ndi woipa; ngakhale wabwino ndi woyera ndi wodetsedwa; ngakhale wopereka nsembe ndi wosapereka konse; wabwino alingana ndi wochimwa; wolumbira ndi woopa lumbira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Anthu onse zimene zidzaŵaonekere nzimodzimodzi, ochita chifuniro cha Mulungu ndi okana omwe, abwino ndi oipa, osamala zachipembedzo ndi osasamala omwe, opereka nsembe ndi osapereka omwe. Wabwino amafanafana ndi woipa. Wochita malumbiro amafanafana ndi woopa kulumbira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Onsewa mathero awo ndi amodzi, anthu olungama ndi anthu oyipa, abwino ndi oyipa, oyera ndi odetsedwa, amene amapereka nsembe ndi amene sapereka nsembe. Zomwe zimachitikira munthu wabwino, zimachitikiranso munthu wochimwa, zomwe zimachitikira amene amalumbira, zimachitikiranso amene amaopa kulumbira. Onani mutuwo |