Mlaliki 9:1 - Buku Lopatulika1 Pakuti zonsezi ndinazisunga mumtima ndikalondoletu zonsezi; kuti olungama ndi anzeru ndi ntchito zao ali m'manja a Mulungu; ngakhale kukonda ngakhale kudana anthu sadziwa; zonse zili m'tsogolo mwao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Pakuti zonsezi ndinazisunga mumtima ndikalondoletu zonsezi; kuti olungama ndi anzeru ndi ntchito zao ali m'manja a Mulungu; ngakhale kukonda ngakhale kudana anthu sadziwa; zonse zili m'tsogolo mwao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Zonse ndanenazi ndidazilingalirapo, ndipo ndidatsimikiza kuti anthu ochita chilungamo ndi anthu anzeru ali m'manja mwa Mulungu pamodzi ndi ntchito zao zomwe. Koma palibe munthu angadziŵe zimene zili m'tsogolo mwake, ngakhale zikhale za chikondi, kapena za chidani. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Ndinalingalira zonse ndanenazi ndipo ndinapeza kuti anthu olungama ndi anthu anzeru ali mʼmanja mwa Mulungu pamodzi ndi zimene amachita, koma palibe amene amadziwa zimene zikumudikira mʼtsogolo mwake, kaya chikondi kapena chidani. Onani mutuwo |