Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 8:17 - Buku Lopatulika

17 pamenepo ndinaona ntchito zonse za Mulungu kuti anthu sangalondole ntchito zichitidwa pansi pano; pakuti angakhale munthu ayesetsa kuzifunafuna koma sadzazipeza; indetu ngakhalenso wanzeru akati, ndidziwa, koma adzalephera kuzilondola.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 pamenepo ndinaona ntchito zonse za Mulungu kuti anthu sangalondole ntchito zichitidwa pansi pano; pakuti angakhale munthu ayesetsa kuzifunafuna koma sadzazipeza; indetu ngakhalenso wanzeru akati, ndidziwa, koma adzalephera kuzilondola.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Ndipo ndidaona ntchito zonse za Mulungu. Palibe munthu amene angathe kuzitulukira zonse zimene zimachitika pansi pano. Ngakhale munthu ayesetse chotani kuzimvetsa, sadzafikapo. Ngakhale munthu wanzeru anene kuti akudziŵa zinthu, nkosatheka kuti azitulukire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 pamenepo ndinaona zonse zimene Mulungu anazichita. Palibe munthu amene angathe kuzimvetsa zonse zimene zimachitika pansi pano. Ngakhale munthu ayesetse kuzifufuza, sangathe kupeza tanthauzo lake. Ngakhale munthu wanzeru atanena kuti iye amadziwa, sangathe kuzimvetsetsa zinthuzo.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 8:17
13 Mawu Ofanana  

amene achita zazikulu ndi zosalondoleka, zinthu zodabwitsa zosawerengeka.


Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.


Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.


Pamene ndinayesa kudziwitsa ichi, ndinavutika nacho;


Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimachitidwa pansi pa thambo; ntchito yovuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.


Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa ntchito za Mulungu amene achita zonse.


Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.


Tapenya ntchito ya Mulungu; pakuti ndani akhoza kulungamitsa chomwe iye anachikhotetsa?


Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.


Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa