Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 8:1 - Buku Lopatulika

1 Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yake, kuduwa kwa nkhope yake ndi kusanduka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yake, kuduwa kwa nkhope yake ndi kusanduka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ndani angafanefane ndi munthu wanzeru? Ndani angadziŵe kutanthauza zinthu? Munthu nzeru zake zimampatsa chimwemwe, ndipo ukali umachoka pankhope pake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndani angafanane ndi munthu wanzeru? Ndani angadziwe kutanthauzira zinthu? Nzeru imabweretsa chimwemwe pa nkhope ya munthu ndipo imasintha maonekedwe ake awukali.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 8:1
27 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tilibe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu.


Akakhala kwa iye mthenga, womasulira mau mmodzi mwa chikwi, kuonetsera munthu chomuyenera;


Ndipo ana a Israele anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso chophimba pankhope pake, kufikira akalowa kulankhula ndi Iye.


kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lake, mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao.


Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yake; koma wokhota mtima adzanyozedwa.


Nzeru ili pamaso pa wozindikira; koma maso a wopusa ali m'malekezero a dziko.


Munthu woipa aumitsa nkhope yake; koma woongoka mtima akonza njira zake.


Mwamuna wanzeru ngwamphamvu; munthu wodziwa ankabe nalimba.


Iye avumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye.


Mfumu inamyankha Daniele, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wovumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kuvumbulutsa chinsinsi ichi.


ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.


Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.


Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse,


Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m'bwalo la akulu a milandu, naona nkhope yake ngati nkhope ya mngelo.


Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, si chifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbumtima.


ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino,


mtundu wa anthu wa nkhope yaukali, wosamalira nkhope ya wokalamba, wosamchitira chifundo mwana;


Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.


ndi kudziwa ichi poyamba, kuti palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa