Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 3:5 - Buku Lopatulika

5 mphindi yakutaya miyala ndi mphindi yakukundika miyala; mphindi yakufungatirana ndi mphindi yakuleka kufungatirana;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 mphindi yakutaya miyala ndi mphindi yakukundika miyala; mphindi yakufungatirana ndi mphindi yakuleka kufungatirana;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pali nthaŵi yokhala malo amodzi ndi nthaŵi yotalikirana, nthaŵi yokumbatirana ndi nthaŵi yoleka zokumbatiranazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Nthawi yotaya miyala ndi nthawi yokundika miyala, nthawi yokumbatirana ndi nthawi yoleka kukumbatirana.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 3:5
11 Mawu Ofanana  

Napasula mizinda, naponya yense mwala wake panthaka ponse pabwino, naidzaza, nafotsera zitsime zonse zamadzi, nagwetsa mitengo yonse yabwino, kufikira anasiya miyala yake mu Kiri-Haresefi mokha; koma oponya miyala anauzinga, naukantha.


Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lachitatu nimusayandikiza mkazi.


mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakuvina;


mphindi yakufunafuna ndi mphindi yakumwazika; mphindi yakusunga ndi mphindi yakutaya;


sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akuluakulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati atuluke m'chipinda mwake, ndi mkwatibwi m'mogona mwake.


Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.


Ndipo kunali, nthawi yakulowa dzuwa, Yoswa analamulira kuti awatsitse kumitengo; ndipo anawataya m'phanga m'mene adabisala; naika miyala yaikulu pakamwa pa phanga, mpaka lero lomwe lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa