8 ndinakundikanso siliva ndi golide ndi chuma cha mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoimbira za mitundumitundu.
8 ndinakundikanso siliva ndi golide ndi chuma cha mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoimbira za mitundumitundu.
8 Ndidaadzikundikiranso siliva ndi golide ndiponso chuma chochokera kwa mafumu amene ndinkaŵalamulira. Ndinali ndi ondiimbira nyimbo, amuna ndi akazi omwe. Ndinalinso ndi akazi aang'ono ochuluka, aja amasangalatsa mitima ya amunaŵa.
8 Ndinadzikundikira siliva ndi golide, ndiponso chuma chochokera kwa mafumu ndi madera awo. Ndinali ndi amuna ndi akazi oyimba ndiponso azikazi; zinthu zokondweretsa mtima wa munthu.
Ndipo mkaziyo ananinkha mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zaunyinji ndi timiyala ta mtengo wapatali; sunafikenso unyinji wotero wa zonunkhira wolingana ndi uja mfumu yaikazi ya ku Sheba inapereka kwa mfumu Solomoni.
Tsono kulemera kwake kwa golide anafika kwa Solomoni chaka chimodzi kunali matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golide.
Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndi zotengera zonse za nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide yekhayekha, panalibe zasiliva, pakuti siliva anangoyesedwa opanda pake masiku onse a Solomoni.
Ndipo Davide ndi akazembe a gulu la nkhondo anapatulira utumikiwo ena a ana a Asafu, ndi a Hemani, ndi a Yedutuni, anenere ndi azeze, ndi zisakasa, ndi nsanje; ndi chiwerengo cha antchito monga mwa kutumikira kwao ndicho:
Onsewa anawalangiza ndi atate wao aimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.
Ndipo mfumu inasema mitengo yambawa ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi azeze, ndi zisakasa za oimbira; sizinaoneke zotere ndi kale lonse m'dziko la Yuda.
osawerenga akapolo ao aamuna ndi aakazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao aamuna ndi aakazi oimbira mazana awiri.