Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 2:7 - Buku Lopatulika

7 ndinadzitengera akapolo ndi adzakazi, ndinali ndi akapolo anabadwa kwanga; ndinalemeranso pokhala nazo zoweta zazikulu ndi zazing'ono kupambana onse anakhala mu Yerusalemu ndisanabadwe ine;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 ndinadzitengera akapolo ndi adzakazi, ndinali ndi akapolo anabadwa kwanga; ndinalemeranso pokhala nazo zoweta zazikulu ndi zazing'ono kupambana onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndidaagula akapolo ndi adzakazi, ndinalinso ndi akapolo obadwira m'nyumba mwanga momwe. Ndinali ndi ng'ombe ndi nkhosa kupambana aliyense amene adalamulirapo ku Yerusalemu kale.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndinagula akapolo aamuna ndi akapolo aakazi, ndiponso ndinali ndi akapolo ena omwe anabadwira mʼnyumba mwanga. Ndinalinso ndi ngʼombe ndi nkhosa zambiri kupambana aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 2:7
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng'ombe ndi siliva ndi golide.


Pamene anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani.


Ndipo Abramu anati, Taonani, simunandipatse ine mbeu; ndipo, taonani, wobadwa m'nyumba mwanga adzalowa m'malo mwanga.


ng'ombe zonenepa khumi, ndi ng'ombe za kubusa makumi awiri, ndi nkhosa zana limodzi, osawerenganso ngondo ndi nswala ndi mphoyo ndi mbalame zoweta.


Ndipo Mesa mfumu ya Mowabu anali mwini nkhosa, akapereka kwa mfumu ya Israele ubweya wa anaankhosa zikwi zana limodzi, ndi wa mphongo zikwi zana limodzi.


Namanga nsanja m'chipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi kunthaka yopatsa bwino; pakuti anakonda kulima.


Ana a akapolo a Solomoni: ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda,


Antchito onse a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri.


Ana a akapolo a Solomoni: ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Perida,


Zoweta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamira zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu aakazi mazana asanu, antchito ake omwe ndi ambiri; chotero munthuyu anaposa anthu onse a kum'mawa.


Ndipo Yehova anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake, ndipo anali nazo nkhosa zikwi khumi ndi zinai, ndi ngamira zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi ng'ombe zamagoli chikwi chimodzi, ndi abulu aakazi chikwi chimodzi.


Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa