Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 10:16 - Buku Lopatulika

16 Tsoka kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana, ndipo akalonga ako adyera mamawa!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Tsoka kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana, ndipo akalonga ako adyera mamawa!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsoka kwa iwe dziko, ngati mfumu yako ikali mwana, ndipo nduna zako zimachezera madyerero usiku wonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Tsoka kwa iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ikali mwana, ndipo atsogoleri ako amakhala pa madyerero mmamawa.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 10:16
16 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu, atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.


Ndipo anamsonkhanira amuna achabe, anthu opanda pake, ndiwo anadzilimbikitsa kutsutsana naye Rehobowamu mwana wa Solomoni, muja Rehobowamu anali mnyamata ndi woolowa mtima, wosakhoza kuwapambana.


Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi,


Yehowahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu miyezi itatu.


Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.


Yehoyakini anali wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu miyezi itatu, ndi masiku khumi; nachita choipa pamaso pa Yehova.


Kalonga wosowa nzeru apambana kusautsa; koma yemwe ada chisiriro adzatanimphitsa moyo wake.


Ntchito ya zitsiru izitopetsa zonsezo, pakuti sichidziwa kunka kumzinda.


Anthu anga awavuta ndi ana, awalamulira ndi akazi. Anthu anga inu, iwo amene akutsogolerani, ndiwo akuchimwitsani, naononga njira zanu zoyendamo.


Nyumba ya Davide iwe, Yehova atero, Chita chiweruzo m'mawa, ndi kumlanditsa amene afunkhidwa m'dzanja la wosautsa, kungatuluke kupsa mtima kwanga ngati moto, ndi kutentha kosazimika, chifukwa cha ntchito zanu zoipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa