Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 10:10 - Buku Lopatulika

10 Chitsulo chikakhala chosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pochenjeza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Chitsulo chikakhala chosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pochenjeza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Nkhwangwa ikakhala yobuntha, nkupandanso kuinola, imalira mphamvu zambiri potema. Koma nzeru zimathandiza munthu kuti athedi kudula kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ngati nkhwangwa ili yobuntha yosanoledwa, pamafunika mphamvu zambiri potema, koma luso limabweretsa chipambano.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 10:10
20 Mawu Ofanana  

Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?


Ndi a ana a Isakara, anthu akuzindikira nyengo, akudziwa zoyenera Israele kuzichita, akulu ao ndiwo mazana awiri; ndi abale ao onse anapenyerera pakamwa pao.


Njoka ikaluma isanalodzedwe, watsenga saona mphotho.


Ntchito ya zitsiru izitopetsa zonsezo, pakuti sichidziwa kunka kumzinda.


Wosendeza miyala adzaphwetekedwa nayo; wowaza nkhuni nadzitema.


Pamenepo ndinazindikira kuti nzeru ipambana utsiru kwambiri, monga kuunika kupambana mdima.


Nzeru ipambana zida za nkhondo; koma wochimwa mmodzi aononga zabwino zambiri.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Pakuti kumvera kwanu kunabuka kwa anthu onse. Chifukwa chake ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pa zabwino, koma ozungulidwa pa zoipa.


Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu.


ndikanola lupanga langa lonyezimira, ndi dzanja langa likagwira chiweruzo; ndidzabwezera chilango ondiukira, ndi kulanga ondida.


Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike.


Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa