Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 7:11 - Buku Lopatulika

11 Tsiku lakumanga malinga ako, tsiku lomwelo lembalo lidzachotsedwa kunka kutali.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Tsiku lakumanga malinga ako, tsiku lomwelo lembalo lidzachotsedwa kunka kutali.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Inu anthu a ku Yerusalemu, idzafikatu nthaŵi yomanganso malinga anu. Nthaŵi imeneyo malire anu adzafutuzidwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Idzafika nthawi yomanganso makoma anu, nthawi yokulitsanso malire anu.

Onani mutuwo Koperani




Mika 7:11
12 Mawu Ofanana  

Pamenepo ndinanena nao, Muona choipa m'mene tilimo, kuti Yerusalemu ali bwinja, ndi zipata zake zotentha ndi moto; tiyeni timange linga la Yerusalemu, tisakhalenso chotonzedwa.


ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya kuzipata za linga lili ku Kachisi, ndi ya linga la mzinda, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira.


Ndipo Tobiya Mwamoni anali naye, nati, Chinkana ichi achimanga, ikakwerako nkhandwe, idzagamula linga lao lamiyala.


Koma tinamanga lingali, ndi linga lonse linalumikizana kufikira pakatimpakati; popeza mitima ya anthu inalunjika kuntchito.


Iwe wosautsidwa, wobelukabeluka ndi namondwe, wosatonthola mtima, taona, ndidzakhazika miyala yako m'mawangamawanga abwino, ndi kukhazika maziko ako ndi masafiro.


Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.


Ndipo iwo amene adzakhala a iwe adzamanga malo akale abwinja; udzautsa maziko a mibadwo yambiri; udzatchedwa Wokonza pogumuka, Wakubwezera njira zakukhalamo.


Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso mizinda yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri.


Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa