Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 6:12 - Buku Lopatulika

12 Pakuti anthu ake olemera adzala ndi chiwawa, ndi okhalamo amanena bodza, ndi lilime lao limachita monyenga m'kamwa mwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pakuti anthu ake olemera adzala ndi chiwawa, ndi okhalamo amanena bodza, ndi lilime lao limachita monyenga m'kamwa mwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Anthu olemera amachita zankhondo. Anthu onse ndi abodza, amangokhalira kunama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Anthu ake olemera amachita zachiwawa; anthu ake ndi abodza ndipo pakamwa pawo pamayankhula zachinyengo.

Onani mutuwo Koperani




Mika 6:12
29 Mawu Ofanana  

Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza, ndi kulilime lonyenga.


Pakuti salankhula zamtendere, koma apangira chiwembu odekha m'dziko.


Koma anamsyasyalika pakamwa pao, namnamiza ndi lilime lao.


Akulu ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera milandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.


Chifukwa kuti Yerusalemu wapasulidwa, ndi Yuda wagwa; chifukwa kuti lilime lao ndi machitidwe ao akana Yehova, kuti autse mkwiyo wa m'maso a ulemerero wake.


Chifukwa kuti munda wampesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israele, ndi anthu a Yuda, mtengo wake womkondweretsa; Iye nayembekeza chiweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza chilungamo, koma onani kufuula.


Lilime lao ndi muvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wake pakamwa pake, koma m'mtima mwake amlalira.


M'mene ndichiritsa Israele, mphulupulu ya Efuremu ivumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti achita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala lilanda kubwalo.


Tsoka kwa iwowa! Pakuti anandizembera; chionongeko kwa iwowa! Pakuti anandilakwira; ndikadawalanditsa Ine, koma anandinenera zabodza.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Yuda, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza akaniza chilamulo cha Yehova, osasunga malemba ake; ndipo awalakwitsa mabodza ao amene makolo ao anawatsata;


ogona pamakama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya anaankhosa a kuzoweta, ndi anaang'ombe ochoka pakati pa khola;


Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha chiundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi chiwawa ndi chinyengo.


Akalonga ake m'kati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.


Ndipo Ayudanso anavomerezana naye, natsimikiza kuti izi zitero.


M'mero mwao muli manda apululu; ndi lilime lao amanyenga; ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa