Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 6:10 - Buku Lopatulika

10 Kodi m'nyumba ya woipa mukali chuma chosalungama, ndi muyeso wochepa umene ayenera kuipidwa nao?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Kodi m'nyumba ya woipa mukali chuma chosalungama, ndi muyeso wochepa umene ayenera kuipidwa nao?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Kodi Ine ndingathe kuiŵala chuma chimene chili m'nyumba za anthu oipa, chimene adachipata monyenga, ndiponso muyeso wopereŵera umene uli wotembereredwa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Inu anthu oyipa, kodi Ine nʼkuyiwala chuma chanu chimene munachipeza mwachinyengo, ndiponso muyeso wanu woperewera umene ndi wotembereredwa?

Onani mutuwo Koperani




Mika 6:10
21 Mawu Ofanana  

Chuma cha uchimo sichithangata; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.


Muyeso wonyenga unyansa Yehova; koma mulingo wamphumphu umsekeretsa.


Miyeso yosiyana, ndi malichero osiyana, zonse ziwirizi zinyansa Yehova.


Miyeso yosiyana inyansa Yehova, ndi mulingo wonyenga suli wabwino.


Kupata chuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.


Pakuti sadziwa kuchita zolungama, amene akundika zachiwawa ndi umbala m'nyumba zao zachifumu, ati Yehova.


Bukitsani kunyumba zachifumu za Asidodi, ndi kunyumba zachifumu za m'dziko la Ejipito, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero aakulu m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwake.


Mau a Yehova aitana mzinda, ndi wanzeru aopa dzina lanu; tamverani ndodo, ndi Iye amene anaiika.


Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha chiundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi chiwawa ndi chinyengo.


Ndipo ndinati, Nchiyani ichi? Nati iye, Ichi ndi efa alikutuluka. Natinso, Ichi ndi maonekedwe ao m'dziko lonse;


Koma ana a Israele analakwa ndi choperekedwacho; popeza Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anatapa choperekedwacho; ndi mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa