Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 8:6 - Buku Lopatulika

6 nati, Ambuye, mnyamata wanga ali gone m'nyumba wodwala manjenje, wozunzidwa koopsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 nati, Ambuye, mnyamata wanga ali gone m'nyumba wodwala manjenje, wozunzidwa koopsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Adampempha kuti, “Ambuye, wantchito wanga ali gone kunyumbaku. Sakutha kuyenda, ndipo akumva kupweteka kwambiri.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 nati, “Ambuye, wantchito wanga ali chigonere ku nyumba, sakuthanso kuyenda, akumva kuwawa kwambiri.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 8:6
12 Mawu Ofanana  

Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamchiritsa iye.


Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.


Ndipo m'mene atachoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka;


Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa inawatulukira, yofuula ndi mau aakulu; ndipo ambiri amanjenje, ndi opunduka, anachiritsidwa.


Ndipo anapeza kumeneko munthu dzina lake Eneya, amene anagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene anagwidwa manjenje.


pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse.


Ambuye inu, chitirani akapolo anu cholungama ndi cholingana; podziwa kuti inunso muli naye Mbuye mu Mwamba.


Ndipo iwo akukhala nao ambuye okhulupirira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupirira ndi okondedwa, oyanjana nao pa chokomacho. Izi uphunzitse, nuchenjeze.


osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa