Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 7:19 - Buku Lopatulika

19 Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino umadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 7:19
13 Mawu Ofanana  

Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.


Anafuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zake, yoyolani masamba ake, mwazani zipatso zake, nyama zakuthengo zichoke pansi pake, ndi mbalame pa nthambi zake.


Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto.


Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma.


Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; chotero mtengo uliwonse wosabala chipatso chabwino udulidwa, nuponyedwa pamoto.


Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipatso.


koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa.


Iwo ndiwo okhala mawanga pa maphwando anu a chikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa