Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 28:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pitani msanga tsono, kauzeni ophunzira ake aja kuti, ‘Iye wauka kwa akufa, ndipo watsogolako kupita ku Galileya, mukamuwonera kumeneko.’ Kumbukirani zimene ndakuuzanizi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndipo pitani msanga kawuzeni ophunzira ake kuti, ‘Wauka kwa akufa ndipo watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona Iye kumeneko.’ Taonani ndakuwuzani.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 28:7
20 Mawu Ofanana  

Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimenezo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine aliponso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindidziwa lililonse.


Nenani inu, tulutsani mlandu wanu; inde, achite uphungu pamodzi; ndani waonetsa ichi chiyambire nthawi yakale? Ndani wanena ichi kale? Kodi si ndine Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine.


Chifukwa chake akanena kwa inu,


Koma nditauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.


Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.


Ndipo iwo anachoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukulu, nathamanga kukauza ophunzira ake.


Komatu nditadzauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.


Iyeyu anapita kuwauza iwo amene ankakhala naye, ali ndi chisoni ndi kulira misozi.


Ndipo iwowa anachoka nawauza otsala; koma iwo omwe sanawavomereze.


nanena, Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni.


Ndipo tsopano ndakuuzani chisanachitike, kuti pamene chitachitika mukakhulupirire.


Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanene kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu.


ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo;


pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa