Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 28:6 - Buku Lopatulika

6 Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Sali muno ai, wauka monga muja adaaneneramu. Bwerani, dzaoneni pamene adaagona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iye muno mulibe, wauka monga mmene ananenera. Bwerani, dzaoneni malo amene anagona.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 28:6
17 Mawu Ofanana  

pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.


Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.


ndipo adzamupha Iye, ndipo Iye adzauka tsiku lachitatu. Ndipo iwo anali ndi chisoni chachikulu.


Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa.


nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.


nanena, Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, Ndidzauka pofika masiku atatu.


Ndipo iye ananena nao, Musadabwe: mulikufuna Yesu Mnazarene amene anapachikidwa; anauka; sali pano; taonani, mbuto m'mene anaikamo Iye!


Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa Munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe aakulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke.


Koma Petro ananyamuka nathamangira kumanda, ndipo powerama anaona nsalu zabafuta pazokha; ndipo anachoka nanka kwao, nazizwa ndi chija chidachitikacho.


ndipo m'mene sanapeze mtembo wake, anadza, nanena kuti adaona m'masomphenya angelo, amene ananena kuti ali ndi moyo Iye.


Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.


Chifukwa cha ichi Atate andikonda Ine, chifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso.


Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani Kachisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa.


yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa