Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 27:66 - Buku Lopatulika

66 Ndipo iwo anamuka, nasunga manda, nasindikizapo chizindikiro pamwalapo, iwo pamodzi ndi alondawo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

66 Ndipo iwo anamuka, nasunga manda, nasindikizapo chizindikiro pamwalapo, iwo pamodzi ndi alondawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

66 Iwo adapitadi, nakatseka manda kolimba posindikiza chizindikiro pa chimwala chotsekeracho. Kenaka adasiya asilikali akulonda pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

66 Tsono anapita nakatseka manda kolimba ndi kuyikapo chizindikiro ndipo anayikapo mlonda.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:66
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenga mwala, nauika pakamwa pa dzenje, niukomera mfumu ndi chosindikizira chake, ndi chosindikizira cha akulu ake, kuti kasasinthike kanthu ka Daniele.


nauika m'manda ake atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo.


Pilato anati kwa iwo, Tengani alonda; mukani, kasungeni monga mudziwa.


Ndipo pamene iwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitidwa.


Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake.


Ndipo pamene anakweza maso anaona kuti mwala wakunkhunizidwa, pakuti unali waukulu ndithu.


Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Maria wa Magadala mamawa, kusanayambe kucha, kumanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda.


Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.


Ndipo Yoswa anati, Kunkhunizirani miyala yaikulu kukamwa kwa phanga, ndi kuikapo anthu, awasunge;


namponya ku chiphompho chakuya, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa