Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 27:3 - Buku Lopatulika

3 Pamenepo Yudasi yemwe anampereka Iye, poona kuti Iye anatsutsidwa kuti afe, analapa, nabweza ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe aakulu ndi akulu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pamenepo Yudasi yemwe anampereka Iye, poona kuti Iye anatsutsidwa kuti afe, analapa, nabweza ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe aakulu ndi akulu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pamene Yudasi, wopereka Yesu kwa adani ake uja, adaona kuti Yesu mlandu wamuipira, nthumanzi idamugwira. Tsono adakaŵabwezera akulu a ansembe ndi akulu a Ayudawo ndalama makumi atatu zasiliva zija.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yudasi, amene anamupereka Iye, ataona kuti Yesu waweruzidwa kuti akaphedwe, anatsutsika mu mtima mwake nakabweza ndalama zamasiliva makumi atatu zija kwa akulu a ansembe ndi kwa akuluakulu.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:3
15 Mawu Ofanana  

kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha, ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi?


Ng'ombeyo ikatunga mnyamata kapena mdzakazi, azipatsa mbuye wake ndalama za masekeli a siliva makumi atatu, ndipo ng'ombeyo aiponye miyala.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Kaziponye kwa woumba mbiya, mtengo wake wokometsetsa anandiyesawo. Ndipo ndinatenga masekeli makumi atatu a siliva, ndi kuziponya kwa woumba mbiya, m'nyumba ya Yehova.


Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,


Ndipo pambuyo pake pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Chimene uchita, chita msanga.


Pamenepo Yudasi, m'mene adatenga gulu la asilikali ndi anyamata, kwa ansembe aakulu ndi Afarisi, anadza komweko ndi nyali ndi miuni ndi zida.


(Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphotho ya chosalungama; ndipo anagwa chamutu, naphulika pakati, ndi matumbo ake onse anakhuthuka;


Pakuti chisoni cha kwa Mulungu chitembenuzira mtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa