Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 27:27 - Buku Lopatulika

27 Pomwepo asilikali a kazembe anamuka naye Yesu kubwalo la milandu, nasonkhanitsa kwa Iye khamu lao lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Pomwepo asilikali a kazembe anamuka naye Yesu kubwalo la milandu, nasonkhanitsa kwa Iye khamu lao lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Pamenepo asilikali a bwanamkubwa adatenga Yesu nakaloŵa naye kunyumba kwa bwanamkubwa. Adasonkhanitsa gulu lonse la asilikali anzao nazinga Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Pamenepo asilikali abwanamkubwayo anamutenga nalowa naye ku bwalo la milandu ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali namuzungulira Iye.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:27
9 Mawu Ofanana  

Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;


Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.


Pamenepo Yudasi, m'mene adatenga gulu la asilikali ndi anyamata, kwa ansembe aakulu ndi Afarisi, anadza komweko ndi nyali ndi miuni ndi zida.


Chifukwa chake Pilato analowanso mu Pretorio, naitana Yesu, nati kwa Iye, Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda kodi?


Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya,


anati, Ndidzamva mlandu wako, pamene akukunenera afika. Ndipo analamulira kuti amdikire iye m'nyumba ya milandu ya Herode.


Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m'ngalawa kunka ku Italiya, anapereka Paulo ndi andende ena kwa kenturiyo dzina lake Julio, wa gulu la Augusto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa