Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 27:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo sanayankhe Iye, ngakhale mau amodzi, kotero kuti kazembe anazizwa ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo sanayankhe Iye, ngakhale mau amodzi, kotero kuti kazembe anazizwa ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Koma Yesu sadamuyankhe kanthu, kotero kuti bwanamkubwa uja adadabwa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Koma Yesu sanayankhe ngakhale mawu amodzi mpaka bwanamkubwa anadabwa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:14
10 Mawu Ofanana  

Ndikhala chodabwitsa kwa ambiri; koma Inu ndinu pothawira panga polimba.


Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tili zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israele, kuchokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m'phiri la Ziyoni.


Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.


Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu.


Ndipo pakumnenera Iye ansembe aakulu ndi akulu, Iye sanayankhe kanthu.


Pomwepo Pilato ananena kwa Iye, Sukumva kodi zinthu zambiri zotere akunenera Iwe?


Koma Yesu sanayankhenso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa.


Ndipo anamfunsa Iye mau ambiri; koma Iye sanamyankhe kanthu.


Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankhe kanthu.


Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa