Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 25:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo opusa anati kwa ochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu zilikuzima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo opusa anati kwa ochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu zilikuzima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Opusa aja adapempha ochenjera aja kuti, ‘Tipatseniko mafuta, onani nyale zathu zikuzima.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Opusawo anati kwa ochenjerawo, ‘Tipatseniko mafuta anu; nyale zathu zikuzima.’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 25:8
18 Mawu Ofanana  

Inde, kuunika kwa woipa kudzazima, ndi lawi la moto wake silidzawala.


Ngati nyali za oipa zizimidwa kawirikawiri? Ngati tsoka lao liwagwera? Ngati Mulungu awagawira zowawa mu mkwiyo wake?


kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu.


Kuunika kwa olungama kukondwa; koma nyali ya oipa idzazima.


Wotemberera atate wake ndi amake, nyali yake idzazima mu mdima woti bii.


Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, natuluka kukakomana ndi mkwati.


Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zao.


Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.


ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana.


Khalani odzimangira m'chuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;


Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto.


Chifukwa chake yang'anirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali nacho; ndipo kwa iye amene alibe chidzachotsedwa, chingakhale chija aoneka ngati ali nacho.


Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.


Chifukwa chake tiope kuti kapena likatsala lonjezano lakulowa mpumulo wake, wina wa inu angaoneke ngati adaliperewera.


Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa