Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 25:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengerenso mafuta;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengeranso mafuta;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta;

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 25:3
12 Mawu Ofanana  

Azindikira kuti malonda ake ampindulira; nyali yake sizima usiku.


Koma iwo andifuna Ine tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera kudziwa njira zanga; monga mtundu wa anthu ochita chilungamo, osasiya chilangizo cha Mulungu wao, iwo andipempha Ine zilangizo zolungama, nakondwerera kuyandikira kwa Mulungu.


nakaona iye lupanga lilikudzera dziko, nakaomba lipenga ndi kuchenjeza anthu;


Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, natuluka kukakomana ndi mkwati.


Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera.


koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao.


akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.


ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba: Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa