Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 24:47 - Buku Lopatulika

47 Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang'anira zinthu zake zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

47 Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang'anira zinthu zake zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

47 Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang'anira chuma chake chonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

47 Zoonadi, ndikuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 24:47
15 Mawu Ofanana  

Mfumu ikomera mtima kapolo wochita mwanzeru; koma idzakwiyira wochititsa manyazi.


Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.


Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero.


Koma kapolo woipa akanena mumtima mwake, Mbuye wanga wachedwa;


Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako.


Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako.


Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.


Ndinena ndinu zoona, kuti adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo.


Ndipo anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'chaching'onong'ono, khala nao ulamuliro pa mizinda khumi.


Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.


ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:


Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.


Iye wakupambana adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndi iye adzakhala mwana wanga.


Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinapambana, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa